print-logo2
A+ A-

Uthenga wabwino wa Yesu | Gospel in Chichewa

pdf

Uthenga Wabwino

–  Chonde werengani izi:

Gen 1:1 Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi
Aroma 3:23  Pakuti onse anachimwa ndikuchepekedwa pa ulemerelo wa Mulungu
Yohane 8:34  Yesu anawayankha, “ indetu indetu, ndinena kwa inu, aliyese wochimwa ndikapolo wa tchimo.

Mulungu anatilenga ife koma sitimudziwa ndipo tinalekanitsidwa ndi iye chifukwa cha uchimo wathu.  Miyoyo yathu popanda Mulungu ilibe tanthawuzo ndi cholinga.  Zotsatira (Chilango) cha uchimo ndi imfa, ku uzimu  ndi kuthupi.  Kufa ku uzimu kukutanthawuza kulekana ndi Mulungu.  Kufa kwa thupi ndikuola kwa thupi.  Tikafa  ndi uchimo tidzalekana kwa muyaya ndi mulungu ndipo tidzapita ku gehena.  Tingadzipulumutse bwanji ku machimo athu ndikubwelera kwa Mulungu?  Sitingadzipulumutse tokha ku machimo athu chifukwa sikotheka kwa munthu wochimwa kudzipulumutsa yekha (monga mmene munthu amene akumira sangadzipulumutse yekha). Tose sitingapulumutsane chifukwa tonse ndife wochimwa (munthu amene akumira sangapulumutse womira mzake, onse akufunika thandizo).  Tikufunika amene alibe tchimo (amene sakumira) kuti atipulumutse ku machimo athu.  Yekhayo wopanda tchimo ndamene angatipulumutse.  Tingamupeze bwanji munthu wopanda tchimo mu dziko la uchimoli limene aliyese ndi wochimwa?

Aroma 6:23 Pakuti mphoto ya uchimo ndi imfa, koma mphatso ya Mulungu ndi moyo wosatha  mwa Mulungu wathu.
Yohane 3:16 Pakuti Mulungu anakonda dziko kotero anapeleka mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyese wokhulupilira iye asataike koma akhale nawo moyo wosatha.
Mateyo 1:23 “ Tawonani, namwali adzakhala ndi mwana, nabala mwana, ndipo adzamutcha Immanuel “, amene akutanthawuza “ Mulungu alinafe”.
Yohane 8:23 Ndipo anawawuza iwo, “ ndinu ochokera pasi; ine ndi ochokera ku mwamba. Ndinu aku dziko; ine si waku dziko ili.
Marko 1:11 Ndipo mawu anachoka kumwamba,  “ uyu ndiye mwana wa Mulungu mwa iyeyu ndikondwera”.
Yohane 8:36 Ndipo ngati mwanayu akupulumutsani, mudzapulumuka ndithu.
Yohane 3:3 Yesu anawayankha nawawuza kuti, “indetu indetu, ndinena ndi inu, ngati simubadwaso mwatsopano, simudzaona ufumu wakumwamba”.
Yohane 1:12 ndipo pamene ambiri  anamulandira, anawapatsa mphavu yokhala ana a Mulungu, kwa amene anakhulupilira dzina lake:

Mulungu,amene anatilenga ife amatikonda kwambiri, anatipatsa yankho.  Kuchokera ku chikondi chake chachikulu pa ife anatuma mwana wake, Yesu, kudzafera machimo athu.  Yesu ndiwopanda tchimo chifukwa sakuchokela ku dziko lapansi, ndipo pamene ali pa dziko, anagonjetsa mayesero a satana a uchimo. Ndi mpulumutsi wa miyoyo yathu (Yesu angathe kutipulumutsa chifukwa sakumira) cholinga cha imfa ya Yesu pa mtanda ndikulipira zochimwa zathu, ndipo, kutichotsa uchimo ndikubwezeletsa ubale wathu ndi Mulungu umene wunanongeka.  Ubale watsopanowu umatchedwa kubadwaso mwa tsopano.  Umabwezeletsa cholinga cha chilengedwe ndi umunthu ndipo, umatipatsa tanthawuzo ndi cholinga chokhalira moyo.

Yohane 11:25 Yesu anati kwa iye, “ ine ndiye kuwukaso ndi moyo. Amene akhulupilira ine ngakhale atafa, adzakhalaso ndi moyo.
Aroma 6:9 Kudziwa Khristu, kuti anawukitsidwa kwa akufa, sadzafaso.  Imfa ilibe ulamuliro pa iye.
Ntchito 2:24 . Amene Mulungu anamuwukitsa kwa akufa, atagonjetsa imfa, chifukwa sikunali kotheka kuti imugonjetse.
Aroma 14:9 Chifukwa Khristu anafa nawukaso, kuti akhale Mbuye wa akufa ndi amoyo.
Ntchito 1:11 Amenenso anati, “ amuna inu a ku galileya, muima bwanji mukuyang’ana ku mwamba? Yesu yemweyu , amene watengedwa kwa inu kupita mwamba, adzabweranso mmonga mene mwamuonera akupita ku mwamba”.

Umboni woti Yesu anapeleka msembe pofera machimo athu unavomelezedwa ndi Mulungu kumwamba?  Umboni uli mukuwukitsidwa kwa Yesu ndi Mulungu.  Pa kuwukitsidwa, zikuwonetsa kuti Yesu anagonjetsa imfa (kapena, mumawu ena, imfa ilibe mphavu pa iye).  Tsopano, kotero, chifukwa yesu  ndi wamoyo. Ifeso titha kukhala ndi moyo.   Moyo wake mwa ife umatipatsa moyo.  Komanso, chifukwa anauka kwa akufa, ndi wamoyo lero.

Yohane 5:24  “ indetu indetu, ndinena ndi inu, iye wakumva mawu anga nakhulupilira amene wandituma adzkahala ndi moyo wosatha ndipo sadzagamulidwa, ndipo adzachoka ku imfa kupita ku moyo.
Yohane 10:9 Ndine Chitseko.  Aliyense wolowa kudzera mwa ine, azapulumutsidwa ndipo azapeza malo abwino.
Yohane 14:6 Yesu anati kwa iwo, “  ine ndine njira, choonadi, ndi moyo. Sungapite kwa tate popanda kudzera kwa ine.
Yohane 8:24 Kotero ndinena ndi inu kuti mudzafa ndi machimo anu; chifukwa simukhulupira kuti ine ndi amene, mudzafa mu machimo anu
Ntchito 4:12 Palibe chipulumutso china, palibe dzina lina limene lapatsidwa kwa anthu limene lingatipulumutse.”
Aroma 10:13 ” Chifukwa “ aliyense woyitanira pa dzina la Mulungu adzapulumutsidwa”
Aroma 10:11 Chifukwa mawu akuti, Aliyese wokhulupilira iye sadzachititsidwa manhyazi”
Aroma 2:11 Palibe kukondera ndi Mulungu.
Aroma 3:22 ngakhale chiyelo cha Mulungu, kudzera mwa Yesu Khristu ndi onse amene akhulupilira. Chifukwa palibe kusiyana;
Aroma 10:9 Ngati mulapa ndi pakamwa panu kuti Yesu ndi Mbuye ndikukhulupilira mu mtima mwanu kuti Mulungu anamuwukitsa kwa akufa, mudzapulumutsidwa.

Machimo athu angachotsedwe bwanji  ndikulanira moyo watsopanowu.  Pokhulupilira mwa yesu ngati Mbuye ndi Mpulumutsi.  Tikalapa machimo athu ndikuitanira pa Yesu kuti atikhululukire ndikutipulumutsa , adzachita izi.  Yesu ndi mwana wa Mulungu amene anabwera ku dziko kudztifela.  Aliyese pa dziko amene atamukhulupilire adzakhululukidwandi Mulungu, adzapulumutsidwa ku machimo awo (ndi ku gehena)  ndikulandira moyo watsopano kuchokera kwa Mulungu.  Mulungu sakondela.  Sakhudzidwa ndi – dziko limene tikukhala, chilankhulo chimene tikulankhula, wolemera kapena wosauka, mwamuna kapena mkazi, wamkulu kapena wang’ono, kapena kusiyana kulikonse.  Aliyense amene akhulupilire ndikulapa kwa Yesu adzapulumutsiwa.  Lotsatilali ndi pemphero limene mungapemphere ngati mukufuna kutsatira Yesu.

Ambuye amene muli ku mwamba, zikomo chifukwa chotumiza mwana wanu wobadwa yekha, Yesu, kudzafera machimo anga kuti ndipulumuke nakhala ndi moyo watsopano wochokera ku mwamba.  Ndikulapa njira zanga ndikupempha chikhululukiro cha machimo anga.  Ndikukhulupilira Yesu ngati Mbuye ndi Mpulumutsi. Ndithandizeni ndi kunditsogolera kukhala moyo wokondwetsa inu mu moyo watsopano umene mwandipatsawu. Amen

Ngati mwapemphera pemphero liri pamwambapa, mufunseni Mulungu akuwonetseni mpingo woti mudizipitako.  Yankhulani ndi Mulungu kudzera mu pemphero nthawi ndi nthawi ndipo Mulungu adziyankhula nanu.   Mverani ku mawu a Mulungu. Mulungu akutsogozani.  Amakukondani ndipo akusamalani.  Mungathe kumukhulupilira. Samalephera kwa iwo amene amamukhulupilira.  Mutha kumudalira pa moyo wanu. Bweretsani zokhumba zanu kwa iye.  Amakukondani ndipo akudalitsani.  Mulungu anati, ‘sindidzakusiyani kapena kukukanani imu’.  Khulupilirani mwa Mulungu. Dalitsikani mwa Yesu.

Werengani Baibulo  nthawi ndi nthawi, kuyambira bukhu la Yohane.  Kuti mudziwe za zambiri za pa internet, dinani apa.